1 Mbiri 14:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Hiramu mfumu ya Turo anatumiza mithenga kwa Davide, ndi mikungudza, ndi amisiri omanga miyala, ndi amatabwa, kuti ammangire nyumba.

2. Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova adamkhazikitsa mfumu ya Israyeli; pakuti ufumu wace unakwezekadi, cifukwa ca anthu ace Israyeli.

3. Ndipo Davide anatenga akazi ena ku Yerusalemu, nabala Davide ana amuna ndi akazi ena.

4. Maina a ana anali nao m'Yerusalemu ndi awa: Samna, ndi Sobabu Natani, ndi Solomo,

5. ndi Ibara, ndi Elisua, ndi Elipeleti,

1 Mbiri 14