32. Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israyeli kuzicita, akuru ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.
33. A Zebuloni akuturuka kukhamu, opangira nkhondo, monga mwa zida ziri zonse za nkhondo, zikwi makumi asanu, akusunga malongosoledwe a nkhondo ndi mtima wosatekeseka.
34. Ndi a Nafitali atsogoleri cikwi cimodzi, ndi pamodzi nao ogwira zikopa ndi mikondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri.
35. Ndi a Adani akupangira nkhondo zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu ndi limodzi.