1. Anadzawo kwa Davide ku Zikilaga, akali citsekedwere cifukwa ca Sauli mwana wa Kisi, ndi awa; ndiwo mwa amphamvuwo omthandiza kunkhondo.
2. Anakoka mauta; naponya miyala, naponya mibvi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe; ndiwo a abale ace a Sauli, Abenjamini.
3. Mkuru wao ndiye Ahiezeri, ndi Yoasi, ana a Semaa wa ku Gibeya; ndi Yezieli, ndi Peleti, ana a Azmaveti; ndi Beraka, ndi Yehu wa ku Anatoti,