1 Mafumu 5:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo mfumu Solomo anasonkhetsa athangata mwa Aisrayeli onse, ndi athangatawo ndiwo anthu zikwi makumi atatu.

14. Ndipo anawatuma ku Lebano mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebano, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata.

15. Ndipo Solomo anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri;

16. osawerenga akapitao a Solomo akuyang'anira nchito, ndiwo zikwi zitatu mphambu mazana atatu, amenewo analamulira anthu aja akugwira nchito.

17. Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuru-ikuru ya mtengo wapatali, kuika maziko ace a nyumbayo ndi miyala yosemasema.

18. Ndipo omanga nyumba a Solomo ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo.

1 Mafumu 5