1 Mafumu 19:20-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndithange ndakapsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera, ndakucitanji?

21. Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yace ndi zipangizo za zocitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.

1 Mafumu 19