7. Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Basa ndi nyumba yace, cifukwa ca zoipa zonse anazicita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wace ndi macitidwe a manja ace, nafanana ndi nyumba ya Yerobiamu; ndiponso popeza anaikantha.
8. Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi ca Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Basa analowa ufumu wa Israyeli ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.
9. Ndipo mnyamata wace Zimri, ndiye woyang'anira dera lina la magareta ace, anampangira ciwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza.
10. Nalowamo Zimri, namkantha, namupha caka ca makomi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwace.
11. Ndipo kunali, atalowa ufumu wace, nakhala pa mpando wacifumu wace, anawakantha onse a m'nyumba ya Basa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ace, kapena wa mabwenzi ace.
12. Motero Zimri anaononga nyumba yonse ya Basa, monga mwa mau a Yehova, amene ananena akumtsutsa Basa, mwa dzanja la Yehu mneneri,