1 Atesalonika 5:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Kondwerani nthawi zonse;

17. Pempherani kosaleka;

18. M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.

19. Musazime Mzimuyo;

20. Musanyoze maaenero;

21. Yesani zonse; sungani cokomaco,

22. Mupewe maonekedwe onse a coipa.

1 Atesalonika 5