1 Atesalonika 1:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'cisautso cambiri, ndi cimwemwe ca Mzimu Woyera;

7. kotero kuti munayamba kukhala inu citsanzo kwa onse akukhulupira m'Makedoniya ndi m'Akaya.

8. Pakuti kuturuka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati m'Makedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse cikhulupiriro canu ca kwa Mulungu cidaturuka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.

9. Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembeoukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weni weni wamoyo,

10. ndi kulindirira Mwana wace acokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife ku mkwiyo ulinkudza.

1 Atesalonika 1