5. Pakuti ngakhalenso iriko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iriko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;
6. koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zicokera kwa iye, ndi ire kufikira kwa iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu, amene zinthu zonse ziri mwa iye, ndi ife mwa iye.
7. Komatu cidziwitso siciri mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo cikumbu mtima cao, popeza ncofoka, cidetsedwa.
8. Koma cakudya sicitibvomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tiribe kupindulako,