30. ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;
31. ndi iwo akucita nalo dziko lapansi, monga ngati osacititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.
32. Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye;
33. koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wace.
34. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso iye wosakwatiwa alabadira za. Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.
35. Koma ici ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakuchereni msampha, koma kukuthandizani kucita cimene ciyenera, ndi kutsata citsatire Ambuye, opanda coceukitsa.