10. Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira nchito ya Ambuye, monganso ine;
11. cifukwa cace munthu asampeputse, Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze: kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale,
12. Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sicinali cifuniro cace kuti adze tsopano, koma adzafika pameneaona nthawi.
13. Dikirani, cirimikani m'cikhulupiriro; dzikhalitseni amuna, limbikani.
14. Zanu zonse zicitike m'cikondi.
15. Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefana, kuti ali cipatsocoundukula ca Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),
16. kuti inunso mubvomere otere, ndi yense wakucita nao, ndi kugwiritsa nchito.