1 Akorinto 15:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. ndi kuti anaikidwa; ndi kutianaukitsidwa tsiku lacitatu, monga mwa malembo;

5. ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;

6. pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ocuruka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;

7. pomwepoanaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa: atumwi onse;

8. ndipo potsiriza pace pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.

9. Pakuti ine ndiri wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kuchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu.

1 Akorinto 15