1. Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe cikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
2. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri naco cikhulupiriro conse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe cikondi, ndiri cabe.
3. Ndipo ndingakhale ndipereka cuma cangaconsekudyetsa osauka, ndipo ndingakhalendipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndiribe cikondi, sindipindula kanthu ai.