1 Akorinto 11:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma ndifunakuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu,

4. Mwamuna yense wobveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wace.

5. Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wobvula mutu, anyoza mutu wace; pakuti kuli cimodzimodzi kumetedwa.

6. Pakuti ngati mkazi sapfunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kucititsa manyazi, apfunde,

7. Pakuti mwamuna sayenera kubvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

8. Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;

9. pakutinso mwamuna sanalengedwa cifukwa ca mkazi;

10. koma mkazi cifukwa ca mwamuna; cifukwa ca ici mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pace, cifukwa ca angelo.

1 Akorinto 11