20. Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.
21. Simungathe kumwera cikho ca Ambuye, ndi cikho ca ziwanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda.
22. Kapena kodi ticititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa iye?
23. Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.
24. Munthu asafune zace za iye yekha, kama za mnzace.
25. Conse cogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu cifukwa ca cikumbu mtima;
26. pakuti dziko lapansi liri la Ambuye, ndi kudzala kwace.
27. Ngati wina wa osakhulupira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye comwe ciikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, cifukwa ca cikumbu mtima.